17 Koma ifeyo abale, pamene tinakakamizika kusiyana nanu kwa nthawi yochepa, tinapitiriza kukukumbukirani ngakhale kuti sitinali kukuonani, ndipo tinayesetsa kwambiri kuti tikwaniritse chilakolako+ chachikulu chimene tinali nacho chofuna kuona nkhope zanu.