15 Pamenepo iye anawauza kuti: “Inu mumadzitcha olungama pamaso pa anthu,+ koma Mulungu akudziwa mitima yanu.+ Chifukwa chimene chili chapamwamba kwa anthu n’chonyansa m’maso mwa Mulungu.+
9 Ndiponso kuti ndikapezeke wogwirizana ndi iye ndikuchita chilungamo. Osati chilungamo changachanga chobwera ndi chilamulo,+ koma chobwera mwa kukhulupirira+ Khristu, chochokera kwa Mulungu pa maziko a chikhulupiriro.+