15 Pakuti mkulu wa ansembe amene tili naye si mkulu wa ansembe amene sangatimvere chisoni+ pa zofooka zathu. Koma tili ndi mkulu wa ansembe amene anayesedwa m’zonse ngati ifeyo, ndipo anakhalabe wopanda uchimo.+
26 Pakuti mkulu wa ansembe ngati ameneyu ndiyedi wotiyenerera.+ Iye ndi wokhulupirika,+ wosalakwa,+ wosaipitsidwa,+ wosiyana ndi anthu ochimwa,+ ndipo wakwera pamwamba kwambiri kuposa kumwamba.+