Miyambo 19:17 Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika 17 Wokomera mtima munthu wonyozeka akukongoza Yehova,+ ndipo adzam’bwezera zimene anachitazo.+ Miyambo 22:9 Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika 9 Wa diso labwino adzadalitsidwa, chifukwa amapereka chakudya chake kwa munthu wonyozeka.+ Mlaliki 11:1 Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika 11 Tumiza mkate wako+ pamadzi,+ chifukwa pakapita masiku ambiri udzaupezanso.+ Luka 6:38 Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika 38 Khalani opatsa ndipo inunso anthu adzakupatsani.+ Adzakhuthulira m’matumba anu muyezo wabwino, wotsendereka, wokhutchumuka ndi wosefukira. Pakuti muyezo umene mukuyezera ena, iwonso adzakuyezerani womwewo.”+
38 Khalani opatsa ndipo inunso anthu adzakupatsani.+ Adzakhuthulira m’matumba anu muyezo wabwino, wotsendereka, wokhutchumuka ndi wosefukira. Pakuti muyezo umene mukuyezera ena, iwonso adzakuyezerani womwewo.”+