Levitiko 25:35 Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika 35 “‘M’bale wanu akasauka pakati panu+ ndipo sangathe kudzisamala, muzim’thandiza.+ Iye ayenera kukhala ndi moyo mmene mlendo wokhala pakati panu+ alili ndi moyo. Deuteronomo 15:7 Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika 7 “Wina mwa abale ako akasauka pakati panu, mu umodzi mwa mizinda yanu, m’dziko limene Yehova Mulungu wako akukupatsa, usamuumire mtima kapena kumuumitsira dzanja lako.+ Salimo 37:26 Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika 26 Tsiku lililonse amakomera mtima ena ndi kuwakongoza zinthu,+Ndipo ana ake adzalandira madalitso.+ Salimo 112:5 Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika 5 Munthu wachisomo+ komanso wokongoza ena zinthu ndi wabwino.+ י [Yohdh]Amachita zinthu mwachilungamo.+ 2 Timoteyo 1:16 Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika 16 Ambuye achitire chifundo banja la Onesiforo,+ chifukwa iye anali kubwera kawirikawiri kudzandilimbikitsa,+ ndipo sanachite manyazi ndi maunyolo anga.+ Aheberi 13:16 Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika 16 Komanso, musaiwale kuchita zabwino+ ndi kugawana zinthu ndi ena, pakuti nsembe zotero Mulungu amakondwera nazo.+
35 “‘M’bale wanu akasauka pakati panu+ ndipo sangathe kudzisamala, muzim’thandiza.+ Iye ayenera kukhala ndi moyo mmene mlendo wokhala pakati panu+ alili ndi moyo.
7 “Wina mwa abale ako akasauka pakati panu, mu umodzi mwa mizinda yanu, m’dziko limene Yehova Mulungu wako akukupatsa, usamuumire mtima kapena kumuumitsira dzanja lako.+
5 Munthu wachisomo+ komanso wokongoza ena zinthu ndi wabwino.+ י [Yohdh]Amachita zinthu mwachilungamo.+
16 Ambuye achitire chifundo banja la Onesiforo,+ chifukwa iye anali kubwera kawirikawiri kudzandilimbikitsa,+ ndipo sanachite manyazi ndi maunyolo anga.+
16 Komanso, musaiwale kuchita zabwino+ ndi kugawana zinthu ndi ena, pakuti nsembe zotero Mulungu amakondwera nazo.+