Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • 1 Samueli 12:3
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 3 Ine ndaima pamaso panu. Munditsutse pamaso pa Yehova ndi pamaso pa wodzozedwa+ wake: Alipo kodi amene ndinam’tengerapo ng’ombe kapena bulu wake?+ Alipo kodi amene ndinam’chitirapo chinyengo, kapena kum’pondereza? Kodi ndinalandirapo chiphuphu kwa aliyense kuti ndisaone zimene anachita?+ Ndili wokonzeka kukubwezerani anthu inu.”+

  • Yobu 1:1
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 1 Kudziko la Uzi+ kunali munthu wina dzina lake Yobu.+ Iye anali munthu wopanda cholakwa,+ wowongoka mtima,+ woopa Mulungu+ ndiponso wopewa zoipa.+

  • Mika 6:8
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 8 Iwe munthu wochokera kufumbi, iye anakuuza zimene zili zabwino.+ Kodi Yehova akufuna chiyani kwa iwe? Iye akufuna kuti uzichita chilungamo,+ ukhale wokoma mtima+ ndiponso uziyenda modzichepetsa+ ndi Mulungu wako.+

  • Mateyu 1:19
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 19 Koma mwamuna wake Yosefe, pokhala munthu wolungama ndiponso posafuna kumuchititsa manyazi kwa anthu,+ anaganiza zomusiya+ mwamseri.*

  • Aefeso 5:15
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 15 Choncho samalani kwambiri kuti mmene mukuyendera+ si monga anthu opanda nzeru, koma ngati anzeru.

  • Akolose 4:5
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 5 Pitirizani kuyenda mwanzeru pochita zinthu ndi anthu akunja,*+ ndipo muzigwiritsa ntchito bwino nthawi yanu.*+

  • 1 Atesalonika 2:10
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 10 Inu ndinu mboni, Mulungunso ndi mboni, za mmene tinakhalira okhulupirika, olungama, ndi opanda chifukwa chotinenezera,+ kwa inu okhulupirira.

Mabuku a Chichewa (1974-2025)
Tulukani
Lowani
  • Chichewa
  • Tumizirani Ena
  • Zimene Mumakonda
  • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
  • Zoyenera Kutsatira
  • Nkhani Yosunga Chinsinsi
  • Privacy Settings
  • JW.ORG
  • Lowani
Tumizirani Ena