Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • Deuteronomo 15:8
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 8 Uzim’kongoza m’bale wako mowolowa manja,+ mulimonse mmene iye wafunira atakupatsa chikole, ndipo uzim’kongoza zimene akusowa.

  • Yobu 31:16
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 16 Ngati ndinkakaniza anthu onyozeka zopempha zawo,+

      Ndipo ngati ndinkachititsa chisoni maso a mkazi wamasiye,+

  • Salimo 37:26
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 26 Tsiku lililonse amakomera mtima ena ndi kuwakongoza zinthu,+

      Ndipo ana ake adzalandira madalitso.+

  • Salimo 41:1
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 41 Wodala ndi munthu amene amachita zinthu moganizira munthu wonyozeka.+

      Pa tsiku la tsoka, Yehova adzamupulumutsa.+

  • Miyambo 14:21
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 21 Munthu wonyoza mnzake ndiye kuti akuchimwa,+ koma wodala ndi munthu wokomera mtima anthu osautsika.+

  • Miyambo 17:5
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 5 Wonyoza munthu wosauka amanyoza amene anam’panga.+ Amene amasangalala ndi tsoka la wina sadzalephera kulangidwa.+

  • Miyambo 19:17
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 17 Wokomera mtima munthu wonyozeka akukongoza Yehova,+ ndipo adzam’bwezera zimene anachitazo.+

  • Miyambo 21:13
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 13 Aliyense wotseka khutu lake kuti asamve kudandaula kwa munthu wonyozeka,+ nayenso adzaitana koma sadzayankhidwa.+

  • Luka 6:35
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 35 Mosiyana ndi zimenezo, inu pitirizani kukonda adani anu. Pitirizani kuchita zabwino, ndi kukongoza+ popanda chiwongoladzanja, osayembekezera kulandira kalikonse. Mukatero, mphoto yanu idzakhala yaikulu ndipo mudzakhala ana a Wam’mwambamwamba,+ chifukwa iye ndi wachifundo+ kwa osayamika ndi kwa oipa.

  • Luka 23:50
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 50 Tsopano panali mwamuna wina dzina lake Yosefe, amene anali wa m’Khoti Lalikulu la Ayuda, munthu wabwino ndi wolungama.+

  • Machitidwe 20:35
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 35 M’zinthu zonse ndakuonetsani kuti mwa kugwira ntchito molimbika chomwechi,+ muthandize ofookawo,+ ndipo muzikumbukira mawu a Ambuye Yesu. Pajatu iye anati, ‘Kupatsa kumabweretsa chimwemwe chochuluka+ kuposa kulandira.’”

  • Aheberi 13:16
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 16 Komanso, musaiwale kuchita zabwino+ ndi kugawana zinthu ndi ena, pakuti nsembe zotero Mulungu amakondwera nazo.+

Mabuku a Chichewa (1974-2025)
Tulukani
Lowani
  • Chichewa
  • Tumizirani Ena
  • Zimene Mumakonda
  • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
  • Zoyenera Kutsatira
  • Nkhani Yosunga Chinsinsi
  • Privacy Settings
  • JW.ORG
  • Lowani
Tumizirani Ena