9 Samala kuti usalankhule mawu achabe mumtima mwako+ kuti, ‘Chaka cha 7, chaka choti anthu angongole amasuke chayandikira,’+ kuti usaolowere manja m’bale wako wosaukayo,+ osam’patsa kalikonse. Pamenepo iye adzafuulira Yehova chifukwa cha zimene iweyo wam’chitira+ ndipo udzapezeka kuti wachimwa.+