Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • Deuteronomo 15:7
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 7 “Wina mwa abale ako akasauka pakati panu, mu umodzi mwa mizinda yanu, m’dziko limene Yehova Mulungu wako akukupatsa, usamuumire mtima kapena kumuumitsira dzanja lako.+

  • Salimo 41:1
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 41 Wodala ndi munthu amene amachita zinthu moganizira munthu wonyozeka.+

      Pa tsiku la tsoka, Yehova adzamupulumutsa.+

  • Miyambo 14:21
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 21 Munthu wonyoza mnzake ndiye kuti akuchimwa,+ koma wodala ndi munthu wokomera mtima anthu osautsika.+

  • Miyambo 19:17
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 17 Wokomera mtima munthu wonyozeka akukongoza Yehova,+ ndipo adzam’bwezera zimene anachitazo.+

  • Miyambo 22:9
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 9 Wa diso labwino adzadalitsidwa, chifukwa amapereka chakudya chake kwa munthu wonyozeka.+

  • Yesaya 58:7
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 7 Ndimafunanso kuti muzigawira chakudya chanu anthu anjala,+ ndiponso kuti muziitanira m’nyumba zanu anthu osautsika ndi osowa pokhala.+ Ndimafuna kuti mukaona munthu wosavala muzimuveka+ ndiponso kuti musamadzibise kwa abale anu.+

  • 2 Akorinto 9:6
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 6 Koma ponena za nkhaniyi, wobzala moumira+ adzakololanso zochepa, ndipo wobzala mowolowa manja+ adzakololanso zochuluka.

  • Aheberi 13:16
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 16 Komanso, musaiwale kuchita zabwino+ ndi kugawana zinthu ndi ena, pakuti nsembe zotero Mulungu amakondwera nazo.+

Mabuku a Chichewa (1974-2025)
Tulukani
Lowani
  • Chichewa
  • Tumizirani Ena
  • Zimene Mumakonda
  • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
  • Zoyenera Kutsatira
  • Nkhani Yosunga Chinsinsi
  • Privacy Settings
  • JW.ORG
  • Lowani
Tumizirani Ena