Salimo 41:1 Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika 41 Wodala ndi munthu amene amachita zinthu moganizira munthu wonyozeka.+Pa tsiku la tsoka, Yehova adzamupulumutsa.+ Salimo 112:9 Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika 9 Iye wagawira ena mowolowa manja, wapereka kwa anthu aumphawi.+ צ [Tsa·dhehʹ]Chilungamo chake chidzakhalapo kwamuyaya.+ ק [Qohph]Nyanga* yake idzakwezedwa ndi ulemerero.+ Miyambo 22:9 Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika 9 Wa diso labwino adzadalitsidwa, chifukwa amapereka chakudya chake kwa munthu wonyozeka.+ Mlaliki 11:1 Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika 11 Tumiza mkate wako+ pamadzi,+ chifukwa pakapita masiku ambiri udzaupezanso.+ Ezekieli 18:7 Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika 7 ngati sazunza munthu aliyense,+ ngati amabweza chikole kwa munthu amene anakongola zinthu zake,+ ngati salanda zinthu za ena mwauchifwamba,+ ngati amapatsa munthu wanjala chakudya+ ndi kuphimba munthu wamaliseche ndi chovala,+ Mateyu 25:35 Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika 35 Pakuti ine ndinamva njala koma inu munandipatsa chakudya.+ Ndinamva ludzu koma inu munandipatsa chakumwa. Ndinali mlendo koma inu munandilandira bwino.+
41 Wodala ndi munthu amene amachita zinthu moganizira munthu wonyozeka.+Pa tsiku la tsoka, Yehova adzamupulumutsa.+
9 Iye wagawira ena mowolowa manja, wapereka kwa anthu aumphawi.+ צ [Tsa·dhehʹ]Chilungamo chake chidzakhalapo kwamuyaya.+ ק [Qohph]Nyanga* yake idzakwezedwa ndi ulemerero.+
7 ngati sazunza munthu aliyense,+ ngati amabweza chikole kwa munthu amene anakongola zinthu zake,+ ngati salanda zinthu za ena mwauchifwamba,+ ngati amapatsa munthu wanjala chakudya+ ndi kuphimba munthu wamaliseche ndi chovala,+
35 Pakuti ine ndinamva njala koma inu munandipatsa chakudya.+ Ndinamva ludzu koma inu munandipatsa chakumwa. Ndinali mlendo koma inu munandilandira bwino.+