Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • Ekisodo 22:23
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 23 Mukamuzunza ngakhale pang’ono, iye n’kundilirira, ndidzamva ndithu kulira kwake.+

  • Deuteronomo 24:15
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 15 Uzim’patsa malipiro ake+ tsiku lililonse, ndipo dzuwa lisalowe usanam’patse malipiro ake chifukwa iye ndi wovutika. Iye akuyembekezera malipiro akewo mwachidwi, ndipo angafuule kwa Yehova chifukwa cha zimene iweyo wam’chitira,+ iwe n’kupezeka kuti wachimwa.+

  • Yobu 34:28
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 28 Kuti achititse kulira kwa wonyozeka kupita kwa iye.

      Choncho iye amamva kulira kwa osautsika.+

  • Miyambo 21:13
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 13 Aliyense wotseka khutu lake kuti asamve kudandaula kwa munthu wonyozeka,+ nayenso adzaitana koma sadzayankhidwa.+

  • Yakobo 5:4
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 4 Tamverani! Malipiro a anthu amene anagwira ntchito+ yokolola m’minda yanu, amene inu simunapereke,+ akufuula ndipo kufuula kwa okololawo kofuna thandizo+ kwafika m’makutu+ a Yehova wa makamu.

Mabuku a Chichewa (1974-2025)
Tulukani
Lowani
  • Chichewa
  • Tumizirani Ena
  • Zimene Mumakonda
  • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
  • Zoyenera Kutsatira
  • Nkhani Yosunga Chinsinsi
  • Privacy Settings
  • JW.ORG
  • Lowani
Tumizirani Ena