Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • Salimo 37:26
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 26 Tsiku lililonse amakomera mtima ena ndi kuwakongoza zinthu,+

      Ndipo ana ake adzalandira madalitso.+

  • Salimo 112:5
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    •  5 Munthu wachisomo+ komanso wokongoza ena zinthu ndi wabwino.+

      י [Yohdh]

      Amachita zinthu mwachilungamo.+

  • Miyambo 3:27
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 27 Usalephere kuchitira zabwino anthu amene akufunikira zabwinozo,+ pamene dzanja lako lingathe kuchita zimenezo.+

  • Miyambo 14:31
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 31 Wobera munthu wosauka mwachinyengo amanyoza amene anamupanga,+ koma wokomera mtima munthu wosauka amalemekeza amene anamupanga.+

  • Luka 6:35
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 35 Mosiyana ndi zimenezo, inu pitirizani kukonda adani anu. Pitirizani kuchita zabwino, ndi kukongoza+ popanda chiwongoladzanja, osayembekezera kulandira kalikonse. Mukatero, mphoto yanu idzakhala yaikulu ndipo mudzakhala ana a Wam’mwambamwamba,+ chifukwa iye ndi wachifundo+ kwa osayamika ndi kwa oipa.

  • Machitidwe 11:29
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 29 Chotero aliyense wa ophunzirawo, anatsimikiza mtima kutumiza thandizo+ lililonse limene akanatha+ kwa abale okhala ku Yudeya.

  • 1 Timoteyo 6:18
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 18 Uwalamule kuti azichita zabwino,+ akhale olemera pa ntchito zabwino,+ owolowa manja, okonzeka kugawira ena,+

  • 1 Yohane 3:17
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 17 Koma aliyense amene ali ndi zinthu zofunika pa moyo,+ n’kuona m’bale wake zikumusowa,+ koma osamusonyeza m’bale wakeyo chifundo chachikulu,+ kodi munthu ameneyu amakonda Mulungu?+

Mabuku a Chichewa (1974-2025)
Tulukani
Lowani
  • Chichewa
  • Tumizirani Ena
  • Zimene Mumakonda
  • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
  • Zoyenera Kutsatira
  • Nkhani Yosunga Chinsinsi
  • Privacy Settings
  • JW.ORG
  • Lowani
Tumizirani Ena