Deuteronomo 24:15 Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika 15 Uzim’patsa malipiro ake+ tsiku lililonse, ndipo dzuwa lisalowe usanam’patse malipiro ake chifukwa iye ndi wovutika. Iye akuyembekezera malipiro akewo mwachidwi, ndipo angafuule kwa Yehova chifukwa cha zimene iweyo wam’chitira,+ iwe n’kupezeka kuti wachimwa.+ Salimo 12:5 Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika 5 Tsopano Yehova wanena kuti: “Chifukwa cha kuponderezedwa kwa osautsika, chifukwa cha kuusa moyo kwa anthu osauka,+Ndidzanyamuka pa nthawiyo,+Ndidzawateteza kwa aliyense wowanyodola.”+ Miyambo 17:5 Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika 5 Wonyoza munthu wosauka amanyoza amene anam’panga.+ Amene amasangalala ndi tsoka la wina sadzalephera kulangidwa.+ Mlaliki 5:8 Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika 8 Ukaona munthu wosauka akuponderezedwa ndiponso zinthu zachiwawa ndi zopanda chilungamo+ zikuchitika m’chigawo cha dziko, usadabwe nazo.+ Pakuti wamkulu kuposa amene akuchita zimenezoyo+ akuona,+ ndipo pamwamba pa akuluakuluwo palinso ena akuluakulu kuposa iwowo. Aroma 15:3 Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika 3 Pakuti ngakhale Khristu sanadzikondweretse yekha,+ koma anachita mmene Malemba amanenera kuti: “Mnyozo wa anthu amene anali kukutonzani wagwa pa ine.”+
15 Uzim’patsa malipiro ake+ tsiku lililonse, ndipo dzuwa lisalowe usanam’patse malipiro ake chifukwa iye ndi wovutika. Iye akuyembekezera malipiro akewo mwachidwi, ndipo angafuule kwa Yehova chifukwa cha zimene iweyo wam’chitira,+ iwe n’kupezeka kuti wachimwa.+
5 Tsopano Yehova wanena kuti: “Chifukwa cha kuponderezedwa kwa osautsika, chifukwa cha kuusa moyo kwa anthu osauka,+Ndidzanyamuka pa nthawiyo,+Ndidzawateteza kwa aliyense wowanyodola.”+
5 Wonyoza munthu wosauka amanyoza amene anam’panga.+ Amene amasangalala ndi tsoka la wina sadzalephera kulangidwa.+
8 Ukaona munthu wosauka akuponderezedwa ndiponso zinthu zachiwawa ndi zopanda chilungamo+ zikuchitika m’chigawo cha dziko, usadabwe nazo.+ Pakuti wamkulu kuposa amene akuchita zimenezoyo+ akuona,+ ndipo pamwamba pa akuluakuluwo palinso ena akuluakulu kuposa iwowo.
3 Pakuti ngakhale Khristu sanadzikondweretse yekha,+ koma anachita mmene Malemba amanenera kuti: “Mnyozo wa anthu amene anali kukutonzani wagwa pa ine.”+