2 Nebukadinezara monga mfumu anatumiza uthenga kwa masatarapi, akuluakulu a boma,+ abwanamkubwa, alangizi, asungichuma, oweruza, akuluakulu apolisi+ ndi oyang’anira onse a zigawo kuti asonkhane ku mwambo wotsegulira+ fano limene mfumu Nebukadinezara inaimika.