25 “Iweyo Ezara, pogwiritsa ntchito nzeru+ zimene Mulungu wako wakupatsa, uike anthu osungitsa malamulo ndi oweruza kuti nthawi zonse aziweruza+ anthu onse a kutsidya lina la Mtsinje, ngakhalenso onse odziwa malamulo a Mulungu wako. Aliyense wosadziwa malamulowo, amuna inu mum’phunzitse.+