22 Amenewa ndiwo aziweruza anthu pa nkhani iliyonse yoyenera. Ndiyeno pakakhala nkhani iliyonse yaikulu azibwera nayo kwa iwe,+ koma nkhani iliyonse yaing’ono, iwo monga oweruza aziisamalira. Choncho amunawo athandizane nawe kunyamula mtolowu, kuti udzipeputsire ntchito.+