Levitiko 25:25 Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika 25 “‘M’bale wanu akasauka n’kugulitsa ena mwa malo ake, wowombola amene ndi wachibale wake wapafupi azibwera ndi kugulanso zimene m’bale wakeyo anagulitsa.+ Deuteronomo 15:7 Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika 7 “Wina mwa abale ako akasauka pakati panu, mu umodzi mwa mizinda yanu, m’dziko limene Yehova Mulungu wako akukupatsa, usamuumire mtima kapena kumuumitsira dzanja lako.+ Salimo 41:1 Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika 41 Wodala ndi munthu amene amachita zinthu moganizira munthu wonyozeka.+Pa tsiku la tsoka, Yehova adzamupulumutsa.+ Miyambo 14:20 Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika 20 Munthu wosauka amadedwa ngakhale ndi mnzake,+ koma munthu wolemera amakhala ndi anzake ambiri.+ Miyambo 17:5 Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika 5 Wonyoza munthu wosauka amanyoza amene anam’panga.+ Amene amasangalala ndi tsoka la wina sadzalephera kulangidwa.+ Miyambo 19:17 Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika 17 Wokomera mtima munthu wonyozeka akukongoza Yehova,+ ndipo adzam’bwezera zimene anachitazo.+ Maliko 14:7 Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika 7 Pakuti osaukawo muli nawo nthawi zonse,+ ndipo nthawi iliyonse imene mwafuna mungathe kuwachitira zabwino. Koma ine simudzakhala nane nthawi zonse.+
25 “‘M’bale wanu akasauka n’kugulitsa ena mwa malo ake, wowombola amene ndi wachibale wake wapafupi azibwera ndi kugulanso zimene m’bale wakeyo anagulitsa.+
7 “Wina mwa abale ako akasauka pakati panu, mu umodzi mwa mizinda yanu, m’dziko limene Yehova Mulungu wako akukupatsa, usamuumire mtima kapena kumuumitsira dzanja lako.+
41 Wodala ndi munthu amene amachita zinthu moganizira munthu wonyozeka.+Pa tsiku la tsoka, Yehova adzamupulumutsa.+
5 Wonyoza munthu wosauka amanyoza amene anam’panga.+ Amene amasangalala ndi tsoka la wina sadzalephera kulangidwa.+
7 Pakuti osaukawo muli nawo nthawi zonse,+ ndipo nthawi iliyonse imene mwafuna mungathe kuwachitira zabwino. Koma ine simudzakhala nane nthawi zonse.+