Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • Ekisodo 22:29
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 29 “Popereka zokolola zako zambirizo komanso zotuluka moponderamo mphesa ndi moyengeramo mafuta zochulukazo, usapereke monyinyirika.+ Mwana wako wamwamuna woyamba kubadwa uzim’pereka kwa ine.+

  • 1 Mbiri 29:17
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 17 Inu Mulungu wanga, ine ndikudziwa bwino kuti inu ndinu wosanthula mitima,+ ndiponso kuti mumakonda chilungamo.+ Ineyo kumbali yanga, ndapereka zinthu zonsezi mwaufulu ndi mtima wowongoka. Ndasangalala kuona anthu anu ali apawa, akupereka zopereka zawo mwaufulu kwa inu.

  • Miyambo 11:25
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 25 Munthu wopatsa mowolowa manja adzalandira mphoto,+ ndipo wothirira ena mosaumira nayenso adzathiriridwa mosaumira.+

  • Machitidwe 20:35
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 35 M’zinthu zonse ndakuonetsani kuti mwa kugwira ntchito molimbika chomwechi,+ muthandize ofookawo,+ ndipo muzikumbukira mawu a Ambuye Yesu. Pajatu iye anati, ‘Kupatsa kumabweretsa chimwemwe chochuluka+ kuposa kulandira.’”

  • Aroma 12:8
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 8 Wochenjeza, aike mtima wake pa kuchenjeza.+ Wogawa, agawe mowolowa manja.+ Wotsogolera,+ atsogolere mwakhama. Ndipo wosonyeza chifundo,+ achite zimenezo mokondwa.

  • Aheberi 13:16
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 16 Komanso, musaiwale kuchita zabwino+ ndi kugawana zinthu ndi ena, pakuti nsembe zotero Mulungu amakondwera nazo.+

Mabuku a Chichewa (1974-2025)
Tulukani
Lowani
  • Chichewa
  • Tumizirani Ena
  • Zimene Mumakonda
  • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
  • Zoyenera Kutsatira
  • Nkhani Yosunga Chinsinsi
  • Privacy Settings
  • JW.ORG
  • Lowani
Tumizirani Ena