1 Atesalonika 5:13 Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika 13 Muwapatse ulemu waukulu mwachikondi chifukwa cha ntchito yawo.+ Khalani mwamtendere pakati panu.+ Yakobo 3:17 Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika 17 Koma nzeru+ yochokera kumwamba, choyamba, ndi yoyera,+ kenako yamtendere,+ yololera,+ yokonzeka kumvera, yodzaza ndi chifundo ndi zipatso zabwino,+ yopanda tsankho,+ ndiponso yopanda chinyengo.+ 1 Petulo 3:11 Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika 11 koma aleke zoipa+ ndipo achite zabwino. Ayesetse kupeza mtendere ndi kuusunga.+ 2 Petulo 3:14 Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika 14 Chotero okondedwa, pakuti mukuyembekezera zinthu zimenezi, chitani chilichonse chotheka kuti iye adzakupezeni opanda banga,+ opanda chilema ndiponso muli mu mtendere.+
17 Koma nzeru+ yochokera kumwamba, choyamba, ndi yoyera,+ kenako yamtendere,+ yololera,+ yokonzeka kumvera, yodzaza ndi chifundo ndi zipatso zabwino,+ yopanda tsankho,+ ndiponso yopanda chinyengo.+
14 Chotero okondedwa, pakuti mukuyembekezera zinthu zimenezi, chitani chilichonse chotheka kuti iye adzakupezeni opanda banga,+ opanda chilema ndiponso muli mu mtendere.+