Salimo 30:3 Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika 3 Inu Yehova, mwanditulutsa m’Manda,+Mwandisunga ndi moyo, kuti ndisatsikire m’dzenje.+ Salimo 34:19 Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika 19 Masoka a munthu wolungama ndi ochuluka,+Koma Yehova amamupulumutsa ku masoka onsewo.+