Yesaya 11:4 Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika 4 Adzaweruza mwachilungamo anthu onyozeka+ ndipo adzadzudzula anthu mowongoka mtima, pothandiza ofatsa a padziko lapansi. Adzakwapula dziko lapansi ndi ndodo ya pakamwa pake,+ ndipo adzagwiritsa ntchito mzimu wa pakamwa pake kupha munthu woipa.+ Chivumbulutso 19:15 Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika 15 M’kamwa mwake munali kutuluka lupanga+ lalitali lakuthwa, loti aphere mitundu ya anthu, ndipo adzawakusa ndi ndodo yachitsulo.+ Iye anali kupondapondanso m’chopondera mphesa+ cha mkwiyo waukulu wa Mulungu+ Wamphamvuyonse.
4 Adzaweruza mwachilungamo anthu onyozeka+ ndipo adzadzudzula anthu mowongoka mtima, pothandiza ofatsa a padziko lapansi. Adzakwapula dziko lapansi ndi ndodo ya pakamwa pake,+ ndipo adzagwiritsa ntchito mzimu wa pakamwa pake kupha munthu woipa.+
15 M’kamwa mwake munali kutuluka lupanga+ lalitali lakuthwa, loti aphere mitundu ya anthu, ndipo adzawakusa ndi ndodo yachitsulo.+ Iye anali kupondapondanso m’chopondera mphesa+ cha mkwiyo waukulu wa Mulungu+ Wamphamvuyonse.