36 Yesu anayankha kuti:+ “Ufumu wanga suli mbali ya dziko lino.+ Ufumu wanga ukanakhala mbali ya dziko lino, atumiki anga akanamenya nkhondo+ kuti ndisaperekedwe kwa Ayuda. Koma ufumu wanga si wochokera pansi pano ayi.”
11 Yesu anamuyankha kuti: “Simukanakhala ndi mphamvu iliyonse pa ine mukanapanda kupatsidwa kuchokera kumwamba.+ Ndiye chifukwa chake munthu amene wandipereka ine kwa inu ali ndi tchimo lalikulu kwambiri.”