3 Kenako Mulungu anadalitsa tsiku la 7. Analipatula kuti likhale lopatulika, chifukwa kuyambira pa tsikuli, iye wakhala akupuma pa ntchito yake yonse yolenga ndi yopanga zimene anafuna.+
11 Pakuti m’masiku 6 Yehova anapanga kumwamba, dziko lapansi, nyanja, ndi zonse zili mmenemo,+ ndipo anayamba kupuma pa tsiku la 7.+ N’chifukwa chake Yehova anadalitsa tsiku la sabata ndi kulipanga kukhala lopatulika.+