15 Kenako, Mose anatembenuka n’kutsika m’phirimo+ atanyamula miyala yosema ya Umboni+ m’manja mwake. Miyalayo inali yolembedwapo mawu mbali zonse ziwiri. Inali yolembedwapo mawu mbali iyi ndi mbali inayo.
10 Mu Likasalo munalibe chilichonse kupatulapo miyala iwiri yosema+ imene Mose anaikamo ku Horebe.+ Anaiikamo nthawi imene Yehova anachita pangano+ ndi ana a Isiraeli, pamene anali kutuluka m’dziko la Iguputo.+