10 Aroni azipaka ena mwa magazi a nyama ya nsembe yamachimo yophimbira machimo,+ panyanga za guwalo kuti aziphimbira machimo. Azichita zimenezi kamodzi pa chaka+ m’mibadwo yanu yonse. Kwa Yehova, guwalo ndi lopatulika koposa.”
14 “Ndiyeno azitenga ena mwa magazi a ng’ombe yamphongoyo,+ ndi kuwadontheza ndi chala chake patsogolo pa chivundikiro, chakum’mawa. Azidontheza+ magaziwo ndi chala chake maulendo 7 patsogolo pa chivundikirocho.+