16 chifukwa kudzera mwa iye+ zinthu zina zonse zinalengedwa, zakumwamba ndi zapadziko lapansi. Inde, zinthu zooneka ndi zinthu zosaoneka, kaya ndi mipando yachifumu, kapena ambuye, kapena maboma, kapena maulamuliro.+ Zinthu zina zonse zinalengedwa kudzera mwa iye,+ ndiponso chifukwa cha iye.