10 Pakuti ngati pamene tinali adani,+ tinayanjanitsidwa kwa Mulungu kudzera mu imfa ya Mwana wake,+ nanji tsopano pamene tayanjanitsidwa, tidzapulumutsidwa ndithu ndi moyo wake.+
18 Koma zinthu zonse n’zochokera kwa Mulungu, amene anatigwirizanitsa+ ndi iyeyo kudzera mwa Khristu, ndipo anatipatsa utumiki+ wokhazikitsanso mtendere.