28 Mukhale tcheru ndi kuyang’anira+ gulu lonse la nkhosa,+ limene mzimu woyera wakuikani pakati pawo kukhala oyang’anira,+ kuti muwete mpingo wa Mulungu,+ umene anaugula ndi magazi+ a Mwana wake weniweni.
2 Wetani+ gulu la nkhosa za Mulungu+ lomwe analisiya m’manja mwanu, osati mokakamizika, koma mofunitsitsa.+ Osatinso chifukwa chofuna kupindulapo kenakake,+ koma ndi mtima wonse.