Numeri 22:7 Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika 7 Chotero, akuluakulu a ku Mowabu ndi a ku Midiyani anapita kwa Balamu+ atatenga malipiro okamulipira kuti awawombezere maula,+ komanso anamuuza zimene Balaki ananena. Numeri 22:21 Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika 21 M’mawa kutacha, Balamu anadzuka n’kumanga chishalo pabulu* wake, ndipo anapita limodzi ndi akalonga a ku Mowabu aja.+ Deuteronomo 23:5 Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika 5 Yehova Mulungu wanu sanafune kumvera Balamu,+ m’malomwake Yehova Mulungu wanu anakusinthirani temberero kukhala dalitso,+ chifukwa Yehova Mulungu wanu anakukondani.+ Nehemiya 13:2 Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika 2 chifukwa iwowa sanachingamire ana a Isiraeli kuti awapatse chakudya+ ndi madzi.+ M’malomwake, analemba ganyu Balamu+ kuti awatemberere.+ Koma Mulungu wathu anasintha temberero limenelo kukhala dalitso.+
7 Chotero, akuluakulu a ku Mowabu ndi a ku Midiyani anapita kwa Balamu+ atatenga malipiro okamulipira kuti awawombezere maula,+ komanso anamuuza zimene Balaki ananena.
21 M’mawa kutacha, Balamu anadzuka n’kumanga chishalo pabulu* wake, ndipo anapita limodzi ndi akalonga a ku Mowabu aja.+
5 Yehova Mulungu wanu sanafune kumvera Balamu,+ m’malomwake Yehova Mulungu wanu anakusinthirani temberero kukhala dalitso,+ chifukwa Yehova Mulungu wanu anakukondani.+
2 chifukwa iwowa sanachingamire ana a Isiraeli kuti awapatse chakudya+ ndi madzi.+ M’malomwake, analemba ganyu Balamu+ kuti awatemberere.+ Koma Mulungu wathu anasintha temberero limenelo kukhala dalitso.+