14Nditayang’ana, ndinaona Mwanawankhosa+ ataimirira paphiri la Ziyoni.+ Limodzi naye panali enanso 144,000+ olembedwa dzina lake ndi dzina la Atate+ wake pamphumi pawo.
3 Iwo anali kuimba+ nyimbo yokhala ngati yatsopano+ pamaso pa mpando wachifumu, pamaso pa zamoyo zinayi,+ ndi pamaso pa akulu.+ Palibe anatha kuiphunzira nyimboyo, koma 144,000+ amene anagulidwa+ padziko lapansi.