11 Chitani zimenezi, makamakanso chifukwa chakuti nyengo ino mukuidziwa, kuti tili kale mu ola lakuti mudzuke ku tulo,+ pakuti chipulumutso chathu chili pafupi kwambiri tsopano kusiyana ndi nthawi imene tinakhala okhulupirira.+
5 inuyo amene Mulungu akukutetezani ndi mphamvu yake chifukwa muli ndi chikhulupiriro.+ Mulungu akukutetezani kuti mudzalandire chipulumutso,+ ndipo chipulumutso chimenechi chidzaonekera+ mu nthawi ya mapeto.+