Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • Malaki 2:16
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 16 Chifukwa ine ndimadana ndi zoti anthu azithetsa mabanja,”+ watero Yehova Mulungu wa Isiraeli. “Ndimadana ndi munthu wankhanza.* Samalani kuti mukhale ndi maganizo oyenera ndipo musamachite zachinyengo,”+ watero Yehova wa magulu ankhondo akumwamba.

  • Mateyu 19:5
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 5 nʼkunena kuti: ‘Chifukwa cha zimenezi mwamuna adzasiya bambo ake ndi mayi ake nʼkudziphatika kwa mkazi wake ndipo awiriwo adzakhala thupi limodziʼ?+

  • Maliko 10:7, 8
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 7 Chifukwa cha zimenezi mwamuna adzasiya bambo ake ndi mayi ake,+ 8 ndipo awiriwo adzakhala thupi limodzi,’+ moti sakhalanso kuti ndi awiri koma thupi limodzi.

  • Aroma 7:2
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 2 Mwachitsanzo, mkazi wokwatiwa amakhala womangidwa kwa mwamuna wake mwalamulo pamene mwamunayo ali moyo. Koma mwamunayo akamwalira, mkazi amakhala womasuka ku lamulo lokhudza mwamuna wake.+

  • 1 Akorinto 6:16
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 16 Kodi inu simukudziwa kuti amene wagonana ndi hule amakhala thupi limodzi ndi huleyo? Chifukwa anati, “Awiriwo adzakhala thupi limodzi.”+

  • Aefeso 5:31
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 31 “Chifukwa cha zimenezi mwamuna adzasiya bambo ake ndi mayi ake nʼkudziphatika kwa* mkazi wake ndipo awiriwo adzakhala thupi limodzi.”+

  • Aheberi 13:4
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 4 Ukwati ukhale wolemekezeka kwa onse, ndipo pogona pa anthu okwatirana pakhale posadetsedwa,+ chifukwa Mulungu adzaweruza achiwerewere* ndiponso achigololo.+

Mabuku a Chichewa (1974-2025)
Tulukani
Lowani
  • Chichewa
  • Tumizirani Ena
  • Zimene Mumakonda
  • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
  • Zoyenera Kutsatira
  • Nkhani Yosunga Chinsinsi
  • Privacy Settings
  • JW.ORG
  • Lowani
Tumizirani Ena