-
Ekisodo 29:36, 37Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
-
-
36 Uzipereka ngʼombe ya nsembe yamachimo tsiku lililonse kuti iphimbe machimo. Uziyeretsa guwa lansembe ku machimo poliperekera nsembe yophimba machimo, ndipo uzilidzoza kuti likhale loyera.+ 37 Udzatenga masiku 7 poperekera guwa lansembelo nsembe yophimba machimo. Udzaliyeretse kuti likhale guwa lansembe loyera koposa.+ Aliyense wogwira guwa lansembe azikhala woyera.
-
-
Levitiko 8:11Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
-
-
11 Anawaza ena mwa mafuta odzozerawo maulendo 7 paguwa lansembe nʼkudzoza guwa lansembelo, zipangizo zake zonse, beseni ndi choikapo chake, kuti zikhale zopatulika.
-