-
Deuteronomo 5:7-10Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
-
-
7 Musakhale ndi milungu ina iliyonse kupatulapo ine.*+
8 Musadzipangire fano kapena chifaniziro+ cha chinthu chilichonse chakumwamba, kapena chapadziko lapansi, kapenanso chamʼmadzi apadziko lapansi. 9 Musaziweramire kapena kuzitumikira,+ chifukwa ine Yehova Mulungu wanu, ndine Mulungu amene ndimafuna kuti anthu azidzipereka kwa ine ndekha,+ amene ndimalanga ana, zidzukulu ndi ana a zidzukuluzo chifukwa cha zolakwa za abambo a anthu odana ndi ine.+ 10 Koma ndimasonyeza chikondi chokhulupirika* kwa anthu mibadwo masauzande amene amandikonda komanso kusunga malamulo anga.
-