-
Ekisodo 36:35, 36Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
-
-
35 Kenako anapanga katani+ ya ulusi wabuluu, ya ubweya wa nkhosa wapepo, ulusi wofiira kwambiri ndi ulusi wopota wabwino kwambiri. Pakataniyo anapetapo+ akerubi.+ 36 Ndiyeno katani imeneyi anaipangira zipilala 4 za mtengo wa mthethe ndipo anazikuta ndi golide. Anapanganso tizitsulo tagolide tokolowekapo katani komanso zitsulo 4 zasiliva zokhazikapo zipilalazo.
-