20 “Iyi ndi nsembe imene Aroni ndi ana ake ayenera kupereka kwa Yehova pa tsiku limene akudzozedwa:+ ufa wosalala wokwana gawo limodzi mwa magawo 10 a muyezo wa efa+ uzikhala nsembe yambewu+ yoperekedwa nthawi zonse. Hafu ya ufawo azipereka mʼmamawa ndipo hafu inayo madzulo.