Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • Ekisodo 29:1, 2
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 29 “Uchite izi kuti uwayeretse kuti atumikire monga ansembe anga: Utenge ngʼombe yaingʼono yamphongo ndi nkhosa ziwiri zamphongo zopanda chilema.+ 2 Utengenso mkate wopanda zofufumitsa, mkate wozungulira woboola pakati wopanda zofufumitsa, wothira mafuta komanso timitanda ta mkate topyapyala topanda zofufumitsa, topaka mafuta.+ Uzipange ndi ufa wa tirigu wosalala.

  • Ekisodo 29:40, 41
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 40 Popereka mwana wa nkhosa woyamba, uzipereka limodzi ndi ufa wosalala, muyezo wake gawo limodzi mwa magawo 10 a muyezo wa efa,* wothira mafuta oyenga bwino kwambiri okwana gawo limodzi mwa magawo 4 a muyezo wa hini,* ndi gawo limodzi mwa magawo 4 a vinyo wa nsembe yachakumwa. 41 Uzipereka mwana wa nkhosa wachiwiri madzulo kuli kachisisira.* Uzimupereka pamodzi ndi nsembe yambewu komanso nsembe yachakumwa ngati mmene unachitira mʼmawa. Uzipereke kuti zikhale kafungo kosangalatsa,* nsembe yowotcha pamoto yoperekedwa kwa Yehova.

  • Levitiko 2:1
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 2 “‘Ngati munthu akupereka nsembe yambewu+ kwa Yehova, azipereka ufa wosalala. Azithira mafuta nʼkuika lubani* pa ufawo.+

  • Levitiko 9:17
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 17 Kenako anapereka nsembe yambewu.+ Anatapako nsembeyo kudzaza dzanja lake nʼkuiwotcha paguwa lansembe, kuwonjezera pa nsembe yopsereza ya mʼmawa.+

  • Numeri 28:4, 5
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 4 Mwana wa nkhosa mmodzi wamphongo muzimupereka nsembe mʼmamawa. Ndipo mwana wa nkhosa wamphongo winayo, muzimupereka nsembe madzulo kuli kachisisira.*+ 5 Muzipereka nsembezi limodzi ndi ufa wosalala wokwana gawo limodzi mwa magawo 10 a muyezo wa efa,* kuti ikhale nsembe yambewu. Ufawo muziuthira mafuta oyenga bwino kwambiri okwana gawo limodzi mwa magawo 4 a muyezo wa hini.*+

Mabuku a Chichewa (1974-2025)
Tulukani
Lowani
  • Chichewa
  • Tumizirani Ena
  • Zimene Mumakonda
  • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
  • Zoyenera Kutsatira
  • Nkhani Yosunga Chinsinsi
  • Privacy Settings
  • JW.ORG
  • Lowani
Tumizirani Ena