-
Ekisodo 29:1-3Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
-
-
29 “Uchite izi kuti uwayeretse kuti atumikire monga ansembe anga: Utenge ngʼombe yaingʼono yamphongo ndi nkhosa ziwiri zamphongo zopanda chilema.+ 2 Utengenso mkate wopanda zofufumitsa, mkate wozungulira woboola pakati wopanda zofufumitsa, wothira mafuta komanso timitanda ta mkate topyapyala topanda zofufumitsa, topaka mafuta.+ Uzipange ndi ufa wa tirigu wosalala. 3 Zimenezi uziike mʼdengu nʼkuzipereka zili mʼdengu momwemo.+ Uchitenso chimodzimodzi ndi ngʼombe ndi nkhosa ziwiri zija.
-
-
Levitiko 6:14, 15Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
-
-
14 Tsopano lamulo la nsembe yambewu+ ndi ili: Ana a Aroni azibweretsa nsembeyi pamaso pa Yehova patsogolo pa guwa lansembe. 15 Mmodzi mwa iwo azitapako ufa wosalala wa nsembe yambewu kudzaza dzanja limodzi komanso azitengako mafuta ake ndi lubani yense amene ali pansembe yambewuyo. Akatero, aziziwotcha paguwa lansembe kuimira nsembe yonseyo kuti zikhale kafungo kosangalatsa* kwa Yehova.+
-