-
Ekisodo 37:25-28Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
-
-
25 Kenako anapanga guwa lansembe zofukiza+ la matabwa a mthethe. Mulitali mwake linali masentimita 45, mulifupi mwake masentimita 45. Mbali zake zonse 4 zinali zofanana, ndipo kutalika kwake kuchoka pansi mpaka mʼmwamba linali masentimita 90. Nyanga zake anazipangira kumodzi ndi guwalo.*+ 26 Analikuta ndi golide woyenga bwino pamwamba pake ndi mʼmbali mwake kuzungulira guwalo komanso nyanga zake. Ndipo anapanga mkombero wagolide kuzungulira guwa lonselo. 27 Anapanga mphete ziwiri zagolide mʼmunsi mwa mkombero kumbali zake ziwiri zoyangʼanizana kuti muzilowa ndodo zonyamulira guwalo. 28 Kenako anapanga ndodo zonyamulira za mtengo wa mthethe ndipo anazikuta ndi golide.
-