-
Ekisodo 30:1-5Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
-
-
30 “Upange guwa lansembe zofukiza.+ Ulipange ndi matabwa amthethe.+ 2 Mbali zake zonse 4 zikhale zofanana, mulitali mwake likhale masentimita 45,* mulifupi mwake masentimita 45. Ndipo kutalika kwake kuchoka pansi mpaka pamwamba likhale masentimita 90. Nyanga zake azipangire kumodzi ndi guwalo.*+ 3 Ulikute ndi golide woyenga bwino pamwamba pake ndi mʼmbali mwake kuzungulira guwalo komanso nyanga zake. Upange mkombero wagolide kuzungulira guwa lonselo. 4 Upangenso mphete ziwiri zagolide mʼmunsi mwa mkombero kumbali zake ziwiri zoyangʼanizana kuti muzilowa ndodo zonyamulira guwalo. 5 Upangenso ndodo zonyamulira za mtengo wa mthethe ndipo uzikute ndi golide.
-