-
Ekisodo 27:1, 2Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
-
-
27 “Upange guwa lansembe lamatabwa a mthethe,+ mulitali likhale mamita awiri,* ndipo mulifupi likhalenso mamita awiri. Guwalo likhale lofanana muyezo wake mbali zake zonse 4, ndipo kutalika kwake kuchokera pansi mpaka mʼmwamba likhale masentimita 134.+ 2 Upange nyanga mʼmakona ake+ 4. Nyangazo zituluke mʼmakonawo ndipo ulikute ndi kopa.*+
-