2 Iwo atenga ena mwa ana aakazi a mitundu inayo kuti akhale akazi awo ndi akazi a ana awo aamuna.+ Anthuwa, omwe ndi ana opatulika,+ asakanikirana ndi anthu a mitundu ina.+ Akalonga komanso atsogoleri ndi amene ali patsogolo kuchita zosakhulupirikazi.”