-
Ekisodo 34:15, 16Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
-
-
15 Samalani kuti musachite pangano ndi anthu okhala mʼdzikomo, chifukwa akamachita uhule ndi milungu yawo komanso kupereka nsembe kwa milungu yawo,+ wina adzakuitanani kunyumba kwake ndipo nanunso mudzadya nsembe yakeyo.+ 16 Kenako mudzatengadi ena mwa ana awo aakazi kuti akhale akazi a ana anu aamuna.+ Ndipo ana awo aakazi adzachita uhule ndi milungu yawo nʼkuchititsa ana anu aamuna kuchita uhule ndi milungu yawo.+
-