Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • Deuteronomo 7:4
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 4 Chifukwa adzachititsa kuti ana anu aamuna asiye kunditsatira ndipo adzatumikira milungu ina.+ Ndiyeno mkwiyo wa Yehova udzakuyakirani ndipo adzakuwonongani mofulumira.+

  • Deuteronomo 31:16
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 16 Tsopano Yehova anauza Mose kuti: “Iweyo watsala pangʼono kufa,* ndipo anthu awa adzakhala osakhulupirika kwa ine ndipo adzayamba kulambira milungu yachilendo imene ili mʼdziko limene akupita.+ Iwo adzandisiya+ nʼkuphwanya pangano limene ndinapangana nawo.+

  • Oweruza 2:17
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 17 Koma Aisiraeli sankamvera oweruzawo. Iwo ankachita chiwerewere ndi milungu ina ndi kuigwadira. Anasiya mwamsanga njira imene makolo awo anayendamo. Makolo awo ankamvera malamulo a Yehova,+ koma iwo sanachite zimenezo.

  • Oweruza 8:33
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 33 Gidiyoni atangomwalira, Aisiraeli anayambanso kulambira Abaala,+ moti anaika Baala-beriti kukhala mulungu wawo.+

  • 1 Mafumu 11:2
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 2 Akaziwa anali ochokera mʼmitundu imene Yehova anauza Aisiraeli kuti: “Musamakwatirane nawo komanso musamacheze nawo, chifukwa adzapotoza mitima yanu kuti muzitsatira milungu yawo.”+ Koma Solomo ankakonda anthu amenewa ndipo sanafune kuwasiya.

  • Nehemiya 13:26
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 26 Kodi si akazi amenewa amene anachimwitsa Solomo mfumu ya Isiraeli? Pa mitundu yonse ya anthu panalibe mfumu yofanana ndi iye.+ Iye ankakondedwa ndi Mulungu wake,+ moti anamuika kukhala mfumu ya Aisiraeli onse. Koma akazi a mitundu ina anamuchimwitsa.+

  • Salimo 106:28
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 28 Kenako iwo anayamba kulambira* Baala wa ku Peori,+

      Ndipo anadya nsembe zoperekedwa kwa akufa.*

Mabuku a Chichewa (1974-2025)
Tulukani
Lowani
  • Chichewa
  • Tumizirani Ena
  • Zimene Mumakonda
  • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
  • Zoyenera Kutsatira
  • Nkhani Yosunga Chinsinsi
  • Privacy Settings
  • JW.ORG
  • Lowani
Tumizirani Ena