8 Ukatero utenge ana ake nʼkuwaveka mikanjo.+ 9 Aroni ndi ana akewo uwamange malamba pamimba. Ana akewo uwakulunge mipango kumutu kwawo ndipo adzakhala ansembe.+ Limeneli ndi lamulo langa mpaka kalekale. Uchite zimenezi kuti uike Aroni ndi ana ake kuti akhale ansembe.+