Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • Ekisodo 29:38-41
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 38 Zimene uzipereka paguwa lansembelo ndi izi: ana a nkhosa a chaka chimodzi, awiri pa tsiku ndipo uzichita zimenezi nthawi zonse.+ 39 Uzipereka mwana wa nkhosa mmodzi mʼmawa, ndipo mwana wa nkhosa winayo madzulo kuli kachisisira.*+ 40 Popereka mwana wa nkhosa woyamba, uzipereka limodzi ndi ufa wosalala, muyezo wake gawo limodzi mwa magawo 10 a muyezo wa efa,* wothira mafuta oyenga bwino kwambiri okwana gawo limodzi mwa magawo 4 a muyezo wa hini,* ndi gawo limodzi mwa magawo 4 a vinyo wa nsembe yachakumwa. 41 Uzipereka mwana wa nkhosa wachiwiri madzulo kuli kachisisira.* Uzimupereka pamodzi ndi nsembe yambewu komanso nsembe yachakumwa ngati mmene unachitira mʼmawa. Uzipereke kuti zikhale kafungo kosangalatsa,* nsembe yowotcha pamoto yoperekedwa kwa Yehova.

  • Numeri 28:4-6
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 4 Mwana wa nkhosa mmodzi wamphongo muzimupereka nsembe mʼmamawa. Ndipo mwana wa nkhosa wamphongo winayo, muzimupereka nsembe madzulo kuli kachisisira.*+ 5 Muzipereka nsembezi limodzi ndi ufa wosalala wokwana gawo limodzi mwa magawo 10 a muyezo wa efa,* kuti ikhale nsembe yambewu. Ufawo muziuthira mafuta oyenga bwino kwambiri okwana gawo limodzi mwa magawo 4 a muyezo wa hini.*+ 6 Imeneyi ndi nsembe yopsereza+ ya tsiku ndi tsiku imene ndinakulamulani kuphiri la Sinai. Ndinakulamulani kuti muziipereka kwa Yehova kuti ikhale nsembe yakafungo kosangalatsa,* yowotcha pamoto.

Mabuku a Chichewa (1974-2025)
Tulukani
Lowani
  • Chichewa
  • Tumizirani Ena
  • Zimene Mumakonda
  • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
  • Zoyenera Kutsatira
  • Nkhani Yosunga Chinsinsi
  • Privacy Settings
  • JW.ORG
  • Lowani
Tumizirani Ena