-
Ekisodo 30:34-36Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
-
-
34 Kenako Yehova anauza Mose kuti: “Utenge muyezo wofanana wa zinthu zonunkhira izi:+ madontho a sitakate,* onika, mafuta onunkhira a galibanamu ndi lubani* weniweni. 35 Zinthu zimenezi upangire zofukiza.+ Usakanize zonunkhiritsa zimenezi mwaluso,* uthire mchere,+ zikhale zoyera ndi zopatulika. 36 Kenako upere zina mwa zofukiza zimenezi kuti zikhale ufa wosalala kwambiri. Uike wina mwa ufawo patsogolo pa Umboni mʼchihema chokumanako, kumene ndidzaonekera kwa iwe. Zofukiza zimenezi zikhale zopatulika koposa kwa inu.
-
-
Chivumbulutso 8:3-5Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
-
-
3 Mngelo wina anafika atanyamula chiwiya chofukizira chagolide nʼkuima paguwa lansembe.+ Iye anapatsidwa zofukiza zambiri+ kuti azipereke nsembe limodzi ndi mapemphero a oyera onse paguwa lansembe lagolide,+ limene linali pamaso pa mpando wachifumu. 4 Utsi wa zofukizazo unakwera pamaso pa Mulungu kuchokera mʼdzanja la mngeloyo limodzi ndi mapemphero+ a oyera. 5 Koma nthawi yomweyo, mngeloyo anatenga chiwiya chofukizira chija nʼkudzazitsamo moto umene anapala paguwa lansembe nʼkuuponyera padziko lapansi. Ndiyeno kunagunda mabingu, kunamveka mawu, kunachita mphezi+ komanso chivomerezi.
-