-
Aheberi 9:24, 25Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
-
-
24 Khristu sanalowe mʼmalo oyera opangidwa ndi manja a anthu,+ amene ndi chithunzi cha malo enieniwo,+ koma analowa kumwamba kwenikweniko.+ Panopa iye ali kumwamba kuti azionekera pamaso pa Mulungu mʼmalo mwa ifeyo.+ 25 Iye sanapite kumwambako kuti azikadzipereka nsembe mobwerezabwereza, ngati mmene mkulu wa ansembe amachitira. Paja mkulu wa ansembe amalowa mʼmalo oyera chaka ndi chaka+ atatenga magazi a nyama, osati ake.
-
-
Aheberi 10:4Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
-
-
4 Chifukwa nʼzosatheka kuti magazi a ngʼombe zamphongo ndi mbuzi achotseretu machimo.
-