-
Levitiko 17:10, 11Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
-
-
10 Munthu aliyense wamʼnyumba ya Isiraeli kapena mlendo wokhala pakati panu, akadya magazi alionse,+ ndidzadana naye ndipo ndidzamupha kuti asakhalenso pakati pa anthu a mtundu wake. 11 Chifukwa moyo wa nyama uli mʼmagazi+ ndipo ine ndawapereka paguwa lansembe+ kuti azikuphimbirani machimo. Zili choncho chifukwa magazi ndi amene amaphimba machimo+ chifukwa cha moyo umene uli mʼmagaziwo.
-