Genesis 9:4 Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika 4 Koma musadye+ nyama limodzi ndi magazi ake,+ chifukwa magaziwo ndi moyo wake. Levitiko 3:17 Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika 17 Musamadye mafuta kapena magazi alionse.+ Limeneli ndi lamulo ku mibadwo yanu yonse mpaka kalekale, kulikonse kumene mungakhale.’” Levitiko 7:26 Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika 26 Musamadye magazi alionse+ kulikonse kumene mungakhale, kaya akhale magazi a mbalame kapena a nyama. Levitiko 19:26 Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika 26 Musamadye chilichonse chimene chili ndi magazi.+ Musamaombeze kapena kuchita zamatsenga.+ 1 Samueli 14:33 Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika 33 Ndiyeno anthu ena anauza Sauli kuti: “Anthutu akuchimwira Yehova. Akudya nyama pamodzi ndi magazi ake.”+ Iye anati: “Mwachita zinthu mopanda chikhulupiriro. Gubuduzani chimwala mubwere nacho kuno mwamsanga.” Machitidwe 15:20 Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika 20 Koma tiyeni tiwalembere kuti apewe zinthu zoipitsidwa ndi mafano,+ chiwerewere,*+ zopotola* ndi magazi.+ Machitidwe 15:29 Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika 29 kupitiriza kupewa zinthu zoperekedwa nsembe kwa mafano,+ magazi,+ zopotola*+ ndi chiwerewere.*+ Mukamapewa zinthu zimenezi mosamala kwambiri, zinthu zidzakuyenderani bwino. Tikukufunirani zabwino zonse!”*
17 Musamadye mafuta kapena magazi alionse.+ Limeneli ndi lamulo ku mibadwo yanu yonse mpaka kalekale, kulikonse kumene mungakhale.’”
26 Musamadye magazi alionse+ kulikonse kumene mungakhale, kaya akhale magazi a mbalame kapena a nyama.
33 Ndiyeno anthu ena anauza Sauli kuti: “Anthutu akuchimwira Yehova. Akudya nyama pamodzi ndi magazi ake.”+ Iye anati: “Mwachita zinthu mopanda chikhulupiriro. Gubuduzani chimwala mubwere nacho kuno mwamsanga.”
20 Koma tiyeni tiwalembere kuti apewe zinthu zoipitsidwa ndi mafano,+ chiwerewere,*+ zopotola* ndi magazi.+
29 kupitiriza kupewa zinthu zoperekedwa nsembe kwa mafano,+ magazi,+ zopotola*+ ndi chiwerewere.*+ Mukamapewa zinthu zimenezi mosamala kwambiri, zinthu zidzakuyenderani bwino. Tikukufunirani zabwino zonse!”*